Blog Detail

Mbiri ya Malemu Fr. Silvestro (Silvio) Zanardi

Fr. Silvestro Zanardi (bambo Silvio) anabadwa pa 28th December 1940 ku Bergamo, m’dziko la Italy. Choncho, bambo Silvio amwalira pa 5 June, 2024 ali ndi zaka  84.

 

Moyo wa unsembe

Bambo Silvio anadzodzedwa unsembe pa 28th June 1967 kwawo ku Italy. Iwo amwalira ali ndi zaka 57 mu unsembe. Mu zaka zimenezi, bambo Silvio atumikira Mulungu ngati wansembe motere:

  • 1971-1977: Burundi
  • 1979-1985: Zambia (Vubwi, Chadiza)
  • 1986: Phalombe, Malawi
  • 1987-1992: Zambia (Chadiza, Mathias Mulumba)
  • 1993: Malawi (Lirangwe)
  • 1999-2024: Malawi (Msamba)

Iwo anatumikira ngati bambo mfumu pa St. John (Msamba) Catholic Parish kuyambira mu chaka cha 2001 mpaka 2012 pamene anapereka udindo wa bambo mfumu kwa Fr. John Paul Somanje. Mu mbiri ya parishi yathu, Bambo Silvio ndi wakhala bambo mfumu kwa zaka zochuluka.

Atapumula pa udindo wa bambo mfumu mu chaka cha 2011, bambo Silvio anapitiriza kutumikira parishi ngati wansembe ongothandiza makamaka ma outstation. Iwo anapitiriza kugwira ntchito yawo ya unsembe yopereka masakaramenti (ubatizo, ukwati, kulapa, kudzoza), kuchita Misa lamulungu/mkati mwa sabata/pamaliro komanso chitukuko. Chitukuko chachikulu chomwe agwira ali wansembe othandiza ndi kumanga tchalitchi latsopano kwa nkhukwa.

 

Tidzawakumbira bwanji?

  • Wansembe ogwira ntchito modzipereka, mosatopa ndi mosayang’anira kukula. Ngakhale nthawi ya covid-19, sanaleke kuchita ngakhale za maliro.
  • Amakondwa pamene mkhristu wabwerera ku masakaramenti komanso kulandira sakaramenti la kulapa
  • Wansembe wamsangala, osakhumudwa msanga, odziwa kukhululuka ndi osasunga mangawa.
  • Wansembe olimbikitsa maphunziro-anamanga sukulu za mkaka (nursery school) ku St. Agness, kwa Chagogo ndi Msampha komwe ndi malo opempherera
  • Anali okonda chitukuko-guwa la panja, mipando ya cement, mipando ya church (pamene Msamba imakondwerera zaka 50 mu chaka cha 2010), church latsopano kwa Nkhukwa
  • Wansembe okonda ana-a Teleza ndi Payomo (Airport, Restaurant)
  • Wansembe odzichepetsa ndi odziwa kugwira bwino ntchito ndi ansembe anzake.

Tipemphe mulungu kuti ntchito zabwino zomwe Bambo Silvio anagwira ali moyo zimuperekeze ku paradizo kwao.