Blog Detail

Ambuye Mwakhwawa Atsogolera Mwambo wa Pelete ya Jubilee ya Wogwira Ntchito za Chitetezo

Episikopi mthandizi wa Arkidayosizi ya Lilongwe, Ambuye Vincent Mwakhwawa apempha ogwira ntchito ku nthambi za chitetezo m’dziko muno kuti akhale akazembe a chiyembekezo pomwe akugwira ntchito zawo.
Ambuye mwakhwawa anena izi masana alero loweruka pa 8 February 2025, pambuyo pa pelete wa akhristu aKatolika amene akugwira ntchito ku nthambi za chitetezo mu arkidayosizi ya Lilongwe, pomwe akukondwelera chaka cha jubile.
Peleteyu anayambila pa bwalo la za masewero la Civo kukafika ku Maula Cathedral, pomwe gulu la asilikali ankhondo, nthambi ya chitetezo ya apolisi, nthambi yowona zolowa ndi kutuluka komanso nthambi ya za m’ndende, ndiwo anatenga nawo gawo pa mwambowu.
Mwazina, Ambuye Mwakhwawa ati nthambizi zili ndi ntchito yaikulu yomwe zimagwira choncho zimafunikira kubwera pamodzi ndikuyambiraso moyo wawo pomwe akukondwelera Chaka Cha Jubilee.
“Amagwira ntchito yolemetsa choncho akufunika chitsogozo cha mzimu woyera.”
M’mawu awo, bambo mlangizi wopuma ku gulu la asilikali ankhondo Colonel Nambo Augustine Machumbuza ati nthambizi zikuyenera kukhala galimoto zonyamulira chikondi komanso chiyembekezo.
Mwazina iwo ati ngati a chitetezo akuyenera kuvala nkhope ya Ambuye yesu pomwe akugwira ntchito yawo.
“Khalani ngati akazembe a ambuye yesu pomwe mukugwira ntchito yanu ndipo mudzinunkhira fungo la chikatolika”
Chikondwelero cha Jubile ya a chitetezo chifika pa chimake mawa ndi mwambo wa msembe ya Misa ku Parish ya St. Ignitious Woyera ku Area 30.
Wolemba ndi Peter Dumayo