MABUNGWE A ACHINYAMATA APEMPHEDWA KUKHALA ODZIDALIRA PA CHUMA
Mpingo waKatolika mu Arkidayosizi ya Lilongwe walangiza achinyamata ake kukhala odzidalira pa kapezedwe ka chuma choyendetsera mabungwe awo mu Arkidayosiziyi.
Ayankhula izi ndi ambuye othandiza a Arkidayosiziyi, ambuye Vincent Fredrick Mwakhwawa pambuyo pa msonkhano omwe anali nawo ndi achinyamatawa Loweruka pa 09 March 2024 ku likulu la Arkidayosiziyi.
Msonkhanowu unakonzedwa ndi cholinga chofuna kukonza mavuto omwe achinyamata akukumana nawo komanso kukonza ndondomeko za mmene angayendere m’chaka cha 2024.
Ambuye Vincent Fredrick Mwakhwawa, ambuye othandiza a Arkidayosizi ya Lilongwe
Mwazina, ambuye Mwakhwawa atsimikizira achinyamatawa kuti ayesetsa kuwaunikira ndi cholinga chofuna kumanga mpingo wa mawa.
Ndipo m’modzi mwa woyang’anira achinyamatawa, Sister Veronica Ng’omba wati nthawi yakwana kuti achinyamatawa ayambe kukhala odzidalira pawokha osati kukhala wopemphapempha.
Sr. Ng’omba ati ali ndi chikhulupiliro chakuti mkumanowu uthandiza kubweretsa achinyamatawa komanso atsogoleri osiyanasiyana pamodzi ndikuthetsa mavuto ochuluka omwe amakumana nawo m’madera omwe akuchokera.
M’modzi mwa woyang’anira achinyamata mu Arkidayosizi ya Lilongwe, Sister Veronica Ng’omba
M’mawu ake, mmodzi mwa achinyamata yemwe anali nawo pa msonkhanowu, Saul Jere wati msonkhanowu uthandizira kuthetsa mavuto omwe analipo pa kayendetsedwe ka mabungwe a achinyamata ponena kuti tsopano apereka nkhawa zawo kwa adindo oyenera.
Jere wati tsopano ali ndi chiyembezo choti mabungwe a chinyamata akhala a mphamvu potsatira msonkhanowu.
Pamsonkhanowu zadziwika kuti achinyamata ambiri satenga nawo gawo komanso sapatsidwa danga lotumikira m’maudindo osiyanasina ku miphakati ndi ku ma parishi omwe amachokera.