Blog Detail

AMBUYE TAMBALA AKHAZIKITSA BUNGWE LA LILONGWE ARCHDIOCESE YOUTH ANIMATION

Gulu lomwe olemekezeka Ambuye George Desmond Tambala alikhazikitsa la Lilongwe Archdiocese Youth Animation lati lionetsetsa kuti umoyo wa achinyamata m’magawo osiyanasiyana maka pankhani zokhudza luso ukupita patsogolo mu Arkidayosiziyi.

M’modzi wa mamembala a gululi yemwe anali wosewera wodziwika bwino kwambiri mdziko muno, Francis Songo ndiye wanena izi Lamulungu la Maitanidwe pa Parishi ya Mlale mu Arkidayosiziyi.

Songo wati gulu lawo muli anthu a maluso osiyanasiyana omwe ali ndi mbiri m’dziko muno ndipo pano akudyelera lusolo kwinaku akutumikira Mulungu.

“Ine m’malo mwa anzanga tasankhidwa ndi Ambuye olemekezeka kuti ngati akatolika komanso aluso losiyanasiyana tithandize achinyamata mu Arkidayosizi yathuyi kupeza maluso awo ndi kudzakhala odzidalira pa mawa. Si onse amene ali ndi nzeru za mkalasi ayi! Ena mwa achinyamatawa ali ndi luso la mpira pamene ena ali ndi maluso a ntchito za manja. Onsewa tikufuna kuwabweretsa pamodzi kuti adziwe zomwe Mulungu adawapatsa. Choncho akadzakhala odzidalira paokha komanso mpingo ndi dziko, zidzapindula,” anatero Songo.

Mmawu ake, mmodzi mwa achinyamata mu Arkidayosiziyi kuchokera ku parishi ya Mkanda, Monica Chibwe wayamikira ambuye Tambala ndi ofesi yawo pokhazikitsa gululi ponena kuti liwathandiza kubweretsa poyera maluso awo poyera ndinso kupititsa patsogolo chikhristu chawo.

“Izi ndi zabwino kwambiri ndipo ife tikuyamika kwambiri potiganizira chonchi. Si tonse amene tili ndi nzeru za mkalasi. Ena tili ndi maluso osiyanasiyana koma timasowa kuti tipita nawo kuti? Kubwera kwa gululi kuthandiza kwambiri. Tikhoza kupempha gululi kuti lidzitipezapeza maparishi mwathumu kuti tikhaledi achinyamata odalilika,” anatero Monica.

Arkiepiskopi wa Arkidayosizi ya Lilongwe, Ambuye Tambala adaganiza zokhazikitsa gululi ndi cholinga choti lidzithandiza achinyamata kumvetsetsa bwino za maitanidwe awo ku mautumiki osiyanasiyana ndi kuzindikira komanso kupititsa patsogolo maluso awo kuti choncho akhale akhristu komanso nzika zodalilika.

Mgululi muli anthu monga Sr. Veronica Ng’omba, Young Chimodzi Snr, Francis Songo komanso Ben Michael mwa ena.

Wolemba ndi Alex Nasoni