Blog Detail

MABUNGWE A ACHINYAMATA APEMPHEDWA KUKHALA OGWILIRA NTCHITO LIMODZI MU MPINGO

Wolemba ndi Titus Jata Phiri
Mabungwe a achinyamata komanso Young Christian Workers (YCW) mu Arkidayosizi yaKatolika ya Lilongwe apemphedwa kuti akhale ogwirana manja pogwira ntchito zawo pamodzi ndicholinga chofuna kupititsa patsogolo mabungwe awo.
Poyankhula pa mkumano womwe mabungwewa anakonza, a Ben Micheal Mankhamba yemwe ndi membala wa komiti yomwe inakonza mkumanowu, wati achinyamata akuyenera kumatula nkhawa zawo kwa adindo maka pa zipsinjo zomwe akukumana nazo.
A Mankhamba alangiza mabungwewa kuti agwiritse ntchito moyenera zomwe zakambidwa pa mkumanowu ndi cholinga chofuna kuthandiza mabungwe awo kuti adziyenda bwino mu Arkidayosiziyi.
“Chomwe tawona ndi choti mabungwe achinyamata akukanika kumanena mavuto omwe akukumana nawo m’mabungwe awo. Nde lero timafuna timve mavuto omwe akukumana nawo, komanso kuthandizana nzeru mwa momwe angayendere chaka chino maka pa nkhani yakapezedwe ka ndalama,” anatero Mankhamba.
Malingana ndi wapampando wa bungwe la Young Christian Workers mu Arkidayosiziyi,John Namalenga Junior wati mkumanowu wawathandiza kulimbikitsa ubale wabungwe lawo ndi bungwe la achinyamata maka pounikira ntchito komanso ndondomeko zomwe atsatire mu chaka cha 2024.
“Mkumano wale lero watithandiza ifeyo ngati a YCW komanso kupanga ubale wa bwino ndi azathu a bungwe la achinyamata ndikubweretsa ntchito zomwe tigwire mchakachi, ngati njira yopezera ndalama zoti zidzithandiza ma bungwe athu m’magawo osiyanasiyana.”
M’mawu ake, wapampando wa bungwe la achinyamata mu arkidayosiziyi, Chisomo Nkhoma, anathokoza akuluakulu kuchokera ku Arkidayosiziyi pochititsa mkumanowu popeza wawatsekula m’maso pa momwe angagwilire ntchito ndi bungwe la YCW komanso momwe angalimbikitsire achinyamata anzawo m’ma parish osiyanasiyana.
Pa mkumanowu panaliso mkulu oyang’anira ma bungwe a achinyamata mu Arkidayosizi ya Lilongwe, Bambo Jean Kesse komanso Sister Veronica Ng’omba mwa ena chabe.