KUKHAZIKITSIDWA KWA THUMBA LOKHALITSA LA TIYENDE LIMODZIENDOWMENT FUND

Ambuye George Desmond Tambala, arkiepiskopi a Arkidayosizi ino ya Lilongwe alemba kalatayi kuti athokoze kwambiri nsembe onse, Asisteri, Ablazala, Akhristu eni ake kudzera ku Miphakati, mabungwe, onse akufuna kwabwino ndi abwenzi a Arkidayosezi ya Lilongwe omwe munatengapo mbali kuti kukhazikitsidwa kwa Tiyende Limodzi Endowment Fund, thumba lokhalitsa, pa 25 July 2026 kuyende bwino, ndipo kuti kuyende mopambana.

Mapemphero anu, kulowa manja kwanu, kudzipereka kwanu, ndi kutenga nawo mbali mwa khama pa Misa yotsegulira ndi nkhomaliro ku Maula Cathedral, komanso pa phwando la madzulo (Legacy Gala Dinner), zasonyeza mgwirizano ndi
kudzipereka kwa tonse ngati banja limodzi la Arkidayosezi yathu ino.

Onani zambiri za chikalatachi kudzera apa.