(+265) 998733593

[email protected]

(+265) 998733593

[email protected]

Blog Detail

Blog Detail

CHAKA CHA BUNGWE LA AMAYI AKATOLIKA : AMAYI AKATOLIKA ADZETSE MTENDERE

  • 25 August 2023

Amayi akatolika kuchokera mu Arkidayosizi ya Lilongwe alimbikitsidwa kupewa mchitidwe wochita zinthu zoipa pomwe akukhala moyo wawo wa tsiku ndi tsiku.

 

Bambo Vincent Mwakhawa ndiwo alimbikitsa amayiwa pomwe amatsekulira msonkhano wa pa chaka wa bungwe la amayi akatolika la CWO, mu Arkidayosizi ya Lilongwe lachinayi pa 24 August 2023 m’boma la Salima.

 

Chaka Chino mwambowu ukukondweleredwa pa mutu woti “Amayi akatolika akhale odzetsa mtendere pakati pa mtundu wa anthu ngati mpingo oyendera limodzi”.

 

Bambo Mwakhawa ayamikira amayi achikatolikawa kamba kotenga nawo gawo muzochitika zosiyanasiyana za mpingo.

 

“Amayi akatolika ndi zida zazikulu kwambri zobweretsa mtendere padziko lapansi lino Kudzela mu mpingo wakatolika pamene tikuyendera limodzi,” atero Bambo Vincent Mwakhawa.

 

M’mawu ake wapampando wa bungweli, mayi Christina Lupiya ati anasankha mutu umenewu kamba koti anaona kuti ndikoyenela kutengela chitsazo cha Mai Maria omwe amadzetsa mtendere pakati pa anthu.

 

“Tisinkhesinkhe kuti kodi ifeyo ngati amayi a mu Arkidayosizi ino ya Lilongwe tikuyenela titani kuti tidzetse mtendere pakati pa mitundu yonse” Mayi Lupiya anayankhula motero.

 

Msonkhanowu wayamba lachinayi pa 24 August ndipo ukuyembekezereka kutha la mulungu pa 27 August 2023.

 

Wolemba: Monicca Chinyama Lipiya