24TH OCTOBER 2026 – FUNDARISING YA ASEMINO
Arkidayosizi ya Lilongwe yati fundraising ya asemino omwe akuchita maphunziro awo m’maseminare osiyanasiyana, idzachitika pa 24 October chaka chino.
Fundraising-yi yakonzedwa pofuna kuthandizira maphunziro a aseminowa pomwe akukonzekera kudzakhala ansembe.
Malingana ndi kalata yomwe ofesi ya mlembi wa a Episikopi a arkidayosiziyi yatulutsa, mwambowu cholinga chake ndi kusonkhanitsa ndalama zothandizira maphunziro a semino omwe akukonzekera kulowa mu utumiki wa unsembe.
Kalatayi yalimbikitsa ma parishi onse omwe sanakwaniritse mulingo omwe anapatsidwa kuti akhale atakwaniritsa mwambowu usanachitike.
Kudzera mu kalatayi, mlembi wa a episkopi, Bambo Peter Makina, apemphanso anthu omwe ali ndikuthekera kuti akhoza kutengapo asemino kuti adziwalipirira maphunziro awo, molingana ndi kuthekera kwawo.
Onani chikalatachi kudzera apa.
